1 AKORINTO 11 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 1Ako. 4.16 Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Khristu.

Za akazi mu Mpingo wa Ambuye

2Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.

3Yoh. 14.28; Aef. 5.23Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.

4Mwamuna yense woveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wake.

5Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.

6Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.

7Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

8Gen. 2.21-22Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;

9Gen. 2.18, 21, 23pakutinso mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi;

10koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo.

11Agal. 3.28Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.

12Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu.

13Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu?

14Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chinyozetsa iye?

15Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.

16Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Mpingo wa Mulungu.

Zosayenera pa madyerero a chikondi. Machitidwe a Mgonero wa Ambuye(Mat. 26.26-29; Mrk. 14.22-25; Luk. 22.14-20)

17Koma pakulalikira ichi sinditama inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choipa.

181Ako. 1.10-12Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndivomereza penapo.

19Mac. 20.30; 1Yoh. 2.19Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu.

20Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;

21pakuti pakudyaku yense ayamba watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.

221Ako. 10.32Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.

23Mat. 26.26-28; 1Ako. 15.3Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;

24Mat. 26.26-28ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.

25Mat. 26.26-28Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa.

26Yoh. 21.22Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.

27Yoh. 13.27Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.

282Ako. 13.5Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho.

29Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.

30Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona.

31Mas. 32.5Koma ngati tikadadzizindikira tokha sitikadaweruzidwa.

32Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.

33Chifukwa chake, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani.

34Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help