2 MBIRI 14 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Asa akantha Akusi

1Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m'mzinda wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake; m'masiku ake dziko linaona bata zaka khumi.

2Ndipo Asa anachita chokoma ndi choyenera m'maso mwa Yehova Mulungu wake,

3nachotsa maguwa a nsembe achilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,

4nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kuchita chilamulo ndi chowauza Iye.

5Anachotsanso m'mizinda yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unachita bata pamaso pake.

6Ndipo anamanga mizinda yamalinga mu Yuda; pakuti dziko linachita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.

7Ndipo anati kwa Yuda, Timange mizinda iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosavutika.

8Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a mu Yuda zikwi mazana atatu; ndi a mu Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.

9Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.

10Natuluka Asa pamaso pake, nanika nkhondoyi m'chigwa cha Zefati ku Maresa.

11Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni.

12Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi.

13Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ake; ndipo anatenga zofunkha zambiri.

14Gen. 35.5Ndipo anakantha mizinda yonse pozungulira pake pa Gerari; pakuti mantha ochokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m'mizinda monse, pakuti mudachuluka zofunkha m'menemo.

15Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndi ngamira; nabwerera kunka ku Yerusalemu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help