HOSEYA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaMneneri Hoseya adalalikira pambuyo pa mneneri Amosi, ku Israele, ufumu wakumpoto, mzinda wa Samariya usanapasuke. Iye amamva chisoni poona kuti Aisraelewo ngosakhulupirika ndi opembedza milungu ina. Tsono anayerekeza kusakhulupirika kwaoko ndi zimene mwiniwakeyo adazipeza m'banja lake, mkazi wake atamchokera nkutsata amuna ena. Chonchonso anthu a Mulunguwo anafulatira Yehova Mbuye wao natsata milungu ina. Mulungu sadzalephera kuwalanga chifukwa cha kusakhulupirika kwaoko; komabe potsiriza, chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, adzawakokeranso kwa Iye ndipo adzayanjana nawonso. Atsimikiza chikondi chakecho ndi mauwa, “Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele…Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi” (11.8).Za mkatimuUkwati wa Hoseya ndi banja lake 1.1—3.5

Mau a Yehova odzudzula Israele 4.1—13.16

Uthenga wa kulapa ndinso lonjezo la kukonzedwanso kwa zinthu 14.1-9

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help