2 MBIRI 8 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Solomoni amanga midzi ina(1Maf. 9.10-28)

1 1Maf. 9.10-28 Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni anamanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba yakeyake,

2Solomoni anamanga mizinda imene Huramu adampatsa, nakhalitsamo ana a Israele.

3Ndipo Solomoni anamuka ku Hamatizoba, naugonjetsa.

4Ndipo anamanga Tadimori m'chipululu, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anaimanga mu Hamati.

5Anamanganso Betehoroni wa kumtunda, ndi Betehoroni wa kunsi, mizinda ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo;

6ndi Baalati, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi mizinda yonse ya magaleta ake, ndi mizinda ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa mu Yerusalemu, ndi mu Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.

7Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisraele,

8mwa ana ao otsala m'dziko pambuyo pao, amene ana a Israele sanawathe, mwa iwowa Solomoni anawachititsa thangata mpaka lero lino.

9Koma mwa ana a Israele Solomoni sanawayese akapolo omgwirira ntchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ake aakulu, ndi akulu a magaleta ake, ndi apakavalo ake.

10Amenewa anali akulu a akapitao a mfumu Solomoni, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu.

11Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mzinda wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.

Malongosoledwe a chipembedzo ndi nsembezo

12Pamenepo Solomoni anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova paguwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo pachipinda cholowera,

13Eks. 29.38; Deut. 16.16monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka: pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa chikondwerero cha Masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa.

141Mbi. 24—26Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.

15Ndipo sanapatuke pa lamulo la mfumu la kwa ansembe ndi Alevi, kunena za kanthu kalikonse, kapena za chumachi.

16Momwemo ntchito yonse ya Solomoni inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza.

17Pamenepo Solomoni anamuka ku Eziyoni-Gebere, ndi ku Eloti m'mphepete mwa nyanja, m'dziko la Edomu.

18Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amalinyero ake, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomoni ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golide, nabwera nao kwa Solomoni mfumu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help