YESAYA 13 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Aneneratu za kuthyoka kwa ufumu wa Babiloni, ndi kubweza Israele kwao

1Katundu wa Babiloni, amene anamuona Yesaya mwana wa Amozi.

2Kwezani mbendera paphiri loti see, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m'zipata za akulu.

3Ine ndalamulira opatulidwa anga, inde, ndaitana amphamvu anga, achite mkwiyo wanga, okondwerera ndi ukulu wanga.

4Yos. 5.13-14Mau a khamu m'mapiri, akunga a mtundu waukulu wa anthu, mau a phokoso la maufumu a mitundu yosonkhanidwa! Yehova wa makamu asonkhanitsa khamu kunkhondo.

5Achokera m'dziko lakutali, kumalekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wake, kuti aononge dziko lonse.

6Zef. 1.7; Yow. 1.15Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova lili pafupi; lidzafika monga chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

7Chifukwa chake manja onse adzafooka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka;

8Yer. 4.31ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.

9Zef. 1.7; Yow. 1.15Taonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali; kupasula dziko, ndi kudzaonongamo akuchimwa psiti.

10Ezk. 32.7; Yow. 2.31; Mat. 24.29Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.

11Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.

12Ndipo ndidzachepsa anthu koposa golide, ngakhale anthu koposa golide weniweni wa ku Ofiri.

13Hag. 2.6Chifukwa chake ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kuchokera m'malo ake, m'mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wake waukali.

14Yer. 50.16; 1Maf. 22.36Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ake, nathawira yense kudziko lake.

15Onse opezedwa adzapyozedwa, ndi onse ogwidwa adzagwa ndi lupanga.

16Zek. 14.2Makanda ao adzatswanyidwe pamaso pao; m'nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndi akazi ao adzakakamizidwa.

17Yer. 51.11, 28Taonani, ndidzawautsira Amedi, amene sadzasamalira siliva, ngakhale golide sadzakondwera naye.

18Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; diso lao silidzaleka ana.

19Yes. 14.4, 22; Gen. 19.24-25Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.

20Yer. 51.37, 43Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo; Mwarabu sadzamanga hema wake pamenepo; abusa sadzagonetsa makamu ao kumeneko.

21Yes. 34.11-15Koma zilombo za m'chipululu zidzagona pamenepo; nyumba zao zidzadzala ndi zakukuwa; ndipo nthiwatiwa zidzakhala pamenepo, ndipo atonde adzajidimuka pamenepo.

22Ndipo mimbulu idzalira m'maboma ao, ndi ankhandwe m'manyumba ao abwino; ndi nthawi yake iyandikira, ndi masiku ake sadzachuluka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help