1 MBIRI 15 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide afikitsa likasa ku Yerusalemu, nalongosola mapembedzedwe

1 1Mbi. 16.1 Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mzinda mwake, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.

2Deut. 10.8Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira Iye kosatha.

31Maf. 8.1Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisraele onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwake adalikonzera.

4Ndipo Davide anasonkhanitsa ana a Aroni ndi Alevi;

5a ana a Kohati, Uriyele mkulu wao, ndi abale ake zana limodzi mphambu makumi awiri;

6a ana a Merari, Asaya mkulu wao, ndi abale ake mazana awiri mphambu makumi awiri;

7a ana a Geresomo, Yowele mkulu wao, ndi abale ake zana limodzi mphambu makumi atatu;

8a ana a Elizafani, Semaya mkulu wao, ndi abale ake mazana awiri;

9a ana a Hebroni, Eliyele mkulu wao, ndi abale ake makumi asanu ndi atatu;

10a ana a Uziyele, Aminadabu mkulu wao, ndi abale ake zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.

11Ndipo Davide anaitana Zadoki ndi Abiyatara ansembe, ndi Alevi Uriyele, Asaya, ndi Yowele, Semaya, ndi Eliyele, ndi Aminadabu, nanena nao,

12Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.

131Mbi. 13.7Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo.

14Momwemo ansembe ndi Alevi anadzipatula kuti akwere nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele.

15Eks. 25.14Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.

16Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe.

171Mbi. 6.33Ndipo Alevi anaika Hemani mwana wa Yowele, ndi a abale ake Asafu mwana wa Berekiya, ndi a ana a Merari, abale ao, Etani mwana wa Kusaya;

18ndi pamodzi nao abale ao a kulongosola kwachiwiri, Zekariya, Beni, ndi Yaaziele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, Eliyabu, ndi Benaya, ndi Maaseiya, ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, odikirawo.

19Oimba tsono: Hemani, Asafu, ndi Etani, anaimba ndi nsanje zamkuwa;

20ndi Zekariya, ndi Aziyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, ndi Eliyabu, ndi Maaseiya, ndi Benaya, ndi zisakasa kuimbira mwa Alimoti;

21ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi Azaziya, ndi azeze akuimbira mwa Seminiti, kutsogolera maimbidwe.

22Ndi Kenaniya mkulu wa Alevi anayang'anira kusenzako; anawalangiza za kusenza, pakuti anali waluso.

23Ndi Berekiya ndi Elikana anali odikira likasa.

24Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netanele, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliyezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obededomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.

252Sam. 6.12-15Momwemo Davide, ndi akuluakulu a Israele, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la chipangano la Yehova, kuchokera kunyumba ya Obededomu mokondwera.

26Ndipo popeza Mulungu anathandiza Alevi akusenza likasa la chipangano la Yehova, iwo anapha nsembe ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.

27Ndipo Davide anavala malaya abafuta, ndi Alevi onse akunyamula likasa, ndi oimba, ndi Kenaniya woyang'anira kusenzaku, pamodzi ndi oimba; Davide anavalanso efodi wabafuta.

28Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.

292Sam. 6.16Ndipo polowa likasa la chipangano la Yehova m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo anasuzumira pazenera, nao mfumu Davide alikutumphatumpha ndi kusewera; ndipo anampeputsa mumtima mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help