1 1Sam. 4.1 Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.
2Ower. 16.23Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo kunyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni.
3Yes. 46.1-2Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwake.
4Yer. 50.2Ndipo m'mawa mwake polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wake ndi zikhato zonse ziwiri za manja ake zinagona zoduka pachiundo; Dagoni anatsala thupi lokha.
5Chifukwa chake angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m'nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa chiundo cha Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino.
Masauko a Afilisti chifukwa cha likasa6Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, mu Asidodi ndi m'midzi yake.
7Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.
8Chifukwa chake anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Israele? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati. Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israele, napita nalo kumeneko.
9Deut. 2.15Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.
10Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu.
111Sam. 5.6, 9Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.
12Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mzindawo kunakwera kumwamba.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.