1Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.
2Ambuye Yehova walumbira pali chiyero chake, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakuchotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza.
3Ndipo mudzatulukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwake, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.
4 Ezk. 20.39; Hos. 12.11 Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu;
5Lev. 7.13nimutenthe nsembe zolemekeza zachotupitsa, nimulalikire nsembe zaufulu, ndi kuzimveketsa; pakuti ichi muchikonda, inu ana a Israele, ati Ambuye Yehova.
6Yer. 5.3Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
7Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mzinda umodzi mvula, osavumbitsira mzinda wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.
8Yer. 5.3M'mwemo mizinda iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumzinda umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
9Deut. 28.22; Yer. 5.3Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
10Deut. 28.27, 60; Yer. 5.3Ndinatumiza mliri pakati panu monga mu Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
11Gen. 19.24-25; Yer. 5.3; Zek. 3.2Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
122Maf. 20.1Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele.
13Mas. 139.2; Yes. 47.4Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.