1Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Yerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israele kulitsutsa;
3nuziti kwa dziko la Israele, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'chimake, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.
4Popeza ndidzakulikhira olungama ndi oipa, chifukwa chake lupanga langa lidzasololokera anthu onse, kuyambira kumwera kufikira kumpoto;
5Ezk. 21.30ndi anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndasolola lupanga langa m'chimake, silidzabwereranso.
6Yes. 22.4Koma wobadwa ndi munthu iwe, usa moyo, ndi kuduka msana, ndi kuwawa mtima, uuse moyo pamaso pao.
7Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo chifukwa ninji? Uzikati, Chifukwa cha mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uliwonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uliwonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona ilinkudza, inde idzachitika, ati Ambuye Yehova.
8Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
9Deut. 32.41Wobadwa ndi munthu iwe, nenera ndi kuti, Atero Ambuye, Nena, Lupanga, lupanga lanoledwa, latuulidwanso;
10lanoledwa kuti liphetu, lituulidwa kuti linge mphezi; tisekererepo kodi? Ndilo ndodo yachifumu ya mwana wanga, yopeputsa mtengo uliwonse.
11Ndipo analipereka alituule, kuti achite nalo lupangali analinola, inde analituula kulipereka m'dzanja la wakupha.
12Fuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israele, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; chifukwa chake panda pantchafu pako.
13Pakuti pali kuyesedwa; ndipo nanga ndodo yachifumu yopeputsa ikapanda kukhalanso? Ati Ambuye Yehova.
14Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitilize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuluyo, limene liwazinga.
15Ndalozetsa nsonga ya lupanga kuzipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kuchuluke; ha! Analituula linyezimire, analisongoza liphe.
16Udzisonkhanitsire pamodzi, muka kudzanja lamanja; undandalitsa nkhondo kumuka kulamanzere; kulikonse ilozako nkhope yako.
17Inenso ndidzaomba manja anga, ndipo ndidzakukwaniritsa ukali wanga; Ine Yehova ndanena.
18Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
19Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babiloni; zonse ziwiri zichokere dziko lomwelo; nulembe chizindikiro cholozera, uchilembe pa mphambano ya njira ya kumzinda.
20Yer. 49.1-6; Ezk. 25.1-5Uiike njira yodzera lupanga kunka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.
21Pakuti mfumu ya ku Babiloni aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mivi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi chiwindi.
22M'dzanja lake lamanja muli ula wa ku Yerusalemu, kuika zogundira, kutsegula pakamwa pa kupha, kukweza mau ndi kufuula, kuikira zitseko zogundira, kuundira mtumbira, kumanga malinga.
23Ndipo kudzakhala ngati kuombeza konyenga pamaso pa iwo amene anawalumbirira malumbiro; koma akumbutsa mphulupulu kuti akodwe.
24Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwakumbutsa mphulupulu yanu povumbuluka zolakwa zanu, kotero kuti machimo anu aoneka m'zonse muzichita, popeza mukumbukika, mudzagwidwa ndi dzanja.
252Mbi. 36.13Ndipo iwe wolasidwa woipa, kalonga wa Israele, amene lafika tsiku lako, nthawi ya mphulupulu yotsiriza;
26Luk. 1.52atero Ambuye Yehova, Chotsa chilemba, vula korona, ufumu sudzakhalanso momwemo, kweza chopepuka, chepsa chokwezeka.
27Gen. 49.10; Luk. 1.32-33; Yoh. 1.49Ndidzagubuduzagubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.
28Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za chitonzo chao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira.
29Akuonera zopanda pake, akuombezera mabodza, lupanga likugoneka pa makosi a oipa olasidwa, amene lafika tsiku lao nthawi ya mphulupulu yotsiriza.
30Yer. 47.6-7Ulibwezere m'chimake. Pamalo unalengedwapo m'dziko la kubadwa kwako ndidzakuweruza.
31Ezk. 7.8Ndipo ndidzakutsanulira mkwiyo wanga, ndidzakuuzira ndi moto wa kuzaza kwanga, ndidzakuperekanso m'manja mwa anthu ankharwe odziwa kuononga.
32Ezk. 25.10Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati padziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndachinena.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.