YEREMIYA 28 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yeremiya atsutsana ndi mneneri wonyenga, Hananiya

1Ndipo panali chaka chomwecho, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, chaka chachinai, mwezi wachisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibiyoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,

2Yer. 27.2, 11-12Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Ndathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.

3Yer. 27.16Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anazichotsa muno, kunka nazo ku Babiloni;

4ndipo ndidzabwezeranso kumalo kuno Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babiloni, ati Yehova: pakuti ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.

5Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa Hananiya mneneri pamaso pa ansembe, ndi pamaso pa anthu onse amene anaima m'nyumba ya Yehova,

6Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am'nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno.

7Koma mumvetu mau awa amene ndinena m'makutu anu, ndi m'makutu a anthu onse:

8Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu aakulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za mliri.

9Deut. 18.22Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzachitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.

10Yer. 27.2Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli pa khosi la Yeremiya, nalithyola.

11Yer. 27.2, 11-12Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Chomwecho ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babiloni zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulichotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anachoka.

12Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, atathyola Hananiya mneneri goli kulichotsa pa khosi la Yeremiya, kuti,

13Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Wathyola magoli amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magoli achitsulo.

14Deut. 28.48; Yer. 27.7Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Ndaika goli lachitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama zakuthengo.

15Ezk. 13.22Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutume iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.

16Deut. 13.5Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.

17Ndipo anafa Hananiya mneneri chaka chomwecho mwezi wachisanu ndi chiwiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help