YESAYA 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Machimo ndi masauko a ana a Israele

1 Num. 12.6; 2Mbi. 26.3-23; 27.1-9; 28.1-27; 29.32 Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.

2 Deut. 32.1, 6, 10, 15 Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.

3Yer. 8.7Ng'ombe idziwa mwini wake, ndi bulu adziwa pomtsekereza: koma Israele sadziwa, anthu anga sazindikira.

4Mat. 3.7Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.

5Yer. 2.30Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.

6Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe changwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.

7Deut. 28.51-52Dziko lanu lili bwinja; mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.

8Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati chitando cha m'munda wampesa, chilindo cha m'munda waminkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.

9Aro. 9.29Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.

Machenjezo ndi maopso a Mulungu

10Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, tcherani makutu ku chilamulo cha Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.

111Sam. 15.22; Mala. 1.10Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde.

12Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna chimenechi m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?

13Num. 28.11Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema misonkhano, sindingalole mphulupulu ndi misonkhano.

14Num. 28.11Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi ya zikondwerero zanu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.

15Mik. 3.4Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.

16Yer. 4.14; Yoh. 5.14Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa;

17Zek. 7.9-10phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.

18 Mas. 51.7; Mik. 6.2 Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.

19Deut. 30.15-18Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,

20koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.

21Mzinda wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.

22Yer. 6.28, 30

Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasakanizidwa ndi madzi.

23Yer. 5.28Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.

24 Ezk. 5.13 Chifukwa chake Ambuye ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga;

25ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzachotsa seta wako wonse:

26Zek. 8.3ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga pachiyambi; pambuyo pake udzatchedwa Mzinda wolungama, mzinda wokhulupirika.

27Ziyoni adzaomboledwa ndi chiweruzo, ndi otembenuka mtima ake ndi chilungamo.

28Mas. 1.6Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ochimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa.

29Chifukwa adzakhala ndi manyazi, chifukwa cha mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, chifukwa cha minda imene mwaisankha.

30Chifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lake linyala, ngatinso munda wopanda madzi.

31Ndimo wamphamvu adzakhala ngati chingwe chathonje, ndi ntchito yake ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help