DEUTERONOMO 8 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Akumbuke zokoma zazikulu Mulungu anawachitira

1Muzisamalira kuchita malamulo onse amene ndikuuzani lero lino, kuti mukhale ndi moyo, ndi kuchuluka, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.

22Mbi. 32.31; Mas. 17.3Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.

3Mat. 4.4Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.

4Neh. 9.21Zovala zanu sizinathe pathupi panu, phazi lanu silinatupe zaka izi makumi anai.

52Sam. 7.14; Miy. 3.12; Aheb. 12.5-6Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.

6Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kumuopa.

7Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe ndi la maiwe akutuluka m'zigwa, ndi m'mapiri;

8dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uchi;

9dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yake nja chitsulo, ndi m'mapiri ake mukumbe mkuwa.

10Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko lokomali anakupatsani.

11Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino;

12kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;

13ndipo zitachuluka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, atachulukanso siliva wanu ndi golide wanu, zitachulukanso zonse muli nazo;

141Ako. 4.7; Mas. 106.21mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo;

15Num. 20.11amene anakutsogolerani m'chipululu chachikulu ndi choopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakutulutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;

16Eks. 16.15amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;

171Ako. 4.7ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira chuma ichi.

18Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitse chipangano chake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino.

19Deut. 30.17-18Ndipo kudzakhala kuti mukaiwalatu Yehova Mulungu wanu, ndi kutsata milungu ina ndi kuitumikira, ndikuchitirani mboni lero lino kuti mudzaonongeka ndithu.

20Monga amitundu amene Yehova awaononga pamaso panu, momwemo mudzaonongeka; chifukwa cha kusamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help