AEFESO 6 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Miy. 23.22; Akol. 3.20 Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino.

2Eks. 20.12Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),

3kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

4Deut. 6.7, 20, 24; Akol. 3.21Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.

5 Akol. 3.22-24 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwa Khristu;

6Akol. 3.22-24si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;

7Akol. 3.22-24akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai;

8Akol. 3.22-24podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.

9Aro. 2.11; Akol. 4.1Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali mu Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye.

Zida za Mulungu

10 Akol. 1.11 Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.

112Ako. 6.7Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.

12Luk. 22.53; Aef. 2.2Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

132Ako. 10.4Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.

14Yes. 11.5; 59.17Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;

15Yes. 52.7ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;

161Yoh. 5.4koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.

17Yes. 59.17; Aheb. 4.12Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;

18Akol. 4.2-4; 1Tim. 2.1mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,

19Akol. 4.2-4; 2Ate. 3.1ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino,

20Akol. 4.2-4chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.

Tikiko apita naye kalatayo

21 Akol. 4.7 Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;

22amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu.

231Pet. 5.14Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.

24Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help