1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2Abwezereni chilango Amidiyani chifukwa cha ana a Israele; utatero udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako.
3Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidiyani, kuwabwezera Amidiyani chilango cha Yehova.
4Muwatume kunkhondo a fuko limodzi, chikwi chimodzi, atere mafuko onse a Israele.
5Ndipo anapereka mwa zikwi za Israele, a fuko limodzi chikwi chimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo.
6Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.
7Ndipo anawathira nkhondo Amidiyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.
8Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.
9Ndipo ana a Israele anagwira akazi a Amidiyani, ndi ana aang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi chuma chao chonse.
10Ndipo anatentha ndi moto mizinda yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.
11Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama.
12Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israele, kuchigono, ku zidikha za Mowabu, zili ku Yordani pafupi pa Yeriko.
Mayeretsedwe a ankhondowo13Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anatuluka kukomana nao kunja kwa chigono.
14Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira.
151Sam. 15.3Ndipo Mose ananena nao, Kodi mwasunga ndi moyo akazi onse?
16Num. 25.2Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.
17Ndipo tsono iphani amuna onse mwa anawo, iphaninso akazi onse akudziwa mwamuna mogona naye.
18Koma ana aakazi onse osadziwa mwamuna mogona naye, asungeni ndi moyo akhale anu.
19Ndipo mukhale m'misasa kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; aliyense adapha munthu, ndi aliyense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lachitatu ndi lachisanu ndi chiwiri, inu ndi andende anu.
20Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo.
21Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la chilamulocho Yehova analamulira Mose ndi ili:
22Golide, ndi siliva, mkuwa, chitsulo, ndolo ndi mtovu zokha,
23Num. 19.19zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi.
24Ndipo mutsuke zovala zanu tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuti mukhale oyera; ndipo mutatero mulowe m'chigono.
Magawidwe a zofunkha25Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
26Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe, ndi Eleazara wansembe, ndi akulu a nyumba za makolo za khamulo;
271Sam. 30.24nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anatuluka kunkhondo, ndi khamu lonse.
28Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akutuluka kunkhondo apereke kwa Yehova: munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.
29Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.
30Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.
31Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe anachita monga Yehova anamuuza Mose.
32Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu,
33ndi ng'ombe zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri,
34ndi abulu zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu chimodzi,
35ndi anthu, ndiwo akazi osadziwa mwamuna mogona naye, onse pamodzi zikwi makumi atatu ndi ziwiri.
36Ndipo limodzi la magawo awiri, ndilo gawo la iwo adatuluka kunkhondo, linafikira nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.
37Ndi msonkho wa Yehova wankhosa ndiwo mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu.
38Ndipo ng'ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri.
39Ndipo abulu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi.
40Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.
41Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.
42Ndipo kunena za gawo la ana a Israele, limene Mose adalichotsa kwa anthu ochita nkhondowo,
43(ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu,
44ndi ng'ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi,
45ndi abulu zikwi makumi atatu ndi mazana asanu,
46ndi anthu zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi,)
47mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
Zopereka zaufulu za akazembe48Pamenepo akazembe a pa ankhondo zikwi, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, anayandikiza kwa Mose;
49nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowe munthu mmodzi wa ife.
50Eks. 30.12Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.
51Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golideyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka.
52Ndipo golide yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.
53Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.
54Eks. 30.16Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku chihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.