1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2Gen. 17.8; Mas. 105.11Uza ana a Israele, nunene nao, Mutalowa m'dziko la Kanani, ndilo dziko logwera inu, likhale cholowa chanu, dziko la Kanani monga mwa malire ake,
3dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum'mawa;
4ndi malire anu adzapinda kuchokera kumwera kunka pokwera Akarabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kutuluka kwake adzachokera kumwera ku Kadesi-Baranea, nadzatuluka kunka ku Hazara-Adara, ndi kupita kunka ku Azimoni;
5ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kunka ku mtsinje wa Ejipito, ndi kutuluka kwao adzatuluka kunyanja.
6Kunena za malire a kumadzulo Nyanja Yaikulu ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.
7Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku Nyanja Yaikulu mulinge kuphiri la Hori:
8kuchokera kuphiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kutuluka kwake kwa malire kudzakhala ku Zedadi.
9Ndipo malirewo adzatuluka kunka ku Zifuroni, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Hazara-Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.
10Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ochokera ku Hazara-Enani kunka ku Sefamu;
11ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
12ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga.
13Yos. 14.1-2Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;
14popeza fuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi hafu la fuko la Manase lalandira cholowa chao;
15mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa.
16Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
17Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale cholowa chanu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
18Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku fuko limodzi, agawe dziko likhale cholowa chao.
19Maina a amunawo ndiwo: wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune.
20Wa fuko la ana a Simeoni, Semuele mwana wa Amihudi.
21Wa fuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni.
22Wa fuko la ana a Dani, kalonga Buki mwana wa Yogili.
23Wa ana a Yosefe; wa fuko la ana a Manase, kalonga Haniyele mwana wa Efodi.
24Wa fuko la ana a Efuremu, kalonga Kemuwele mwana wa Sifutani.
25Wa fuko la ana a Zebuloni, kalonga Elizafani mwana wa Paranaki.
26Wa fuko la ana a Isakara, kalonga Palatiele mwana wa Azani.
27Wa fuko la ana a Asere, kalonga Ahihudi mwana wa Selomi.
28Wa fuko la ana a Nafutali, kalonga Pedahele mwana wa Amihudi.
29Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israele cholowa chao m'dziko la Kanani.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.