1 2Sam. 11.1; 12.26-31 Ndipo kunali, pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Yowabu anatsogolera khamu lamphamvu, napasula dziko la ana a Amoni, nadza, naumangira misasa Raba. Koma Davide anakhala ku Yerusalemu. Ndipo Yowabu anakantha Raba, naupasula.
2Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumchotsa pamutu pake, napeza kulemera kwake talente wa golide; panalinso miyala ya mtengo wake pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, natulutsa zankhondo za m'mzindamo zambiri ndithu.
3Natulutsanso anthu anali m'mwemo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi zipangizo zochekera zachitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi mizinda yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu.
Abwereza kukantha Afilisti(2Sam. 21.15-22)4 2Sam. 21.18-22 Ndipo zitatha izi, inauka nkhondo ku Gezere ndi Afilisti; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Sipai wa ana a chimphona; ndipo anawagonjetsa.
5Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliyati Mgiti, amene luti la mkondo wake linanga mtanda woombera nsalu.
6Ndipo panalinso nkhondo ku Gati; kumeneko kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene zala zake za kumanja ndi kumapazi ndizo makumi awiri mphambu zinai; zisanu ndi chimodzi ku dzanja lililonse, ndi zisanu ndi chimodzi ku phazi lililonse; nayenso anabadwa mwa chimphonacho.
7Ndipo potonza Israele iyeyu Yonatani mwana wa Simea mbale wake wa Davide anamkantha.
8Awa anabadwa mwa chimphonacho ku Gati, koma anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.