1 Yes. 57.1 Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;
pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu.
2 Mas. 144.8; Yer. 9.8 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake,
amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.
3 Mas. 144.8; Yer. 9.8 Yehova adzadula milomo yonse yothyasika,
lilime lakudzitamandira;
4amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;
milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?
5 Eks. 3.7-8 Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika,
chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi,
ndiuka tsopano, ati Yehova;
ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
6 Mas. 19.8-9 Mau a Yehova ndi mau oona;
ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi,
yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.
7Mudzawasunga, Yehova,
mudzawatchinjirizira mbadwo uno kunthawi zonse.
8Oipa amayenda mozungulirazungulira,
potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.