1Iwo akukhulupirira Yehova
akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.
2Monga mapiri azinga Yerusalemu,
momwemo Yehova azinga anthu ake,
kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
3 Yes. 14.5 Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama;
kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.
4Chitirani chokoma, Yehova, iwo okhala okoma;
iwo okhala oongoka mumtima mwao.
5 Miy. 2.15; Agal. 6.16 Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota,
Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake.
Mtendere ukhale pa Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.