1 Miy. 22.1 Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.
2Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.
32Ako. 7.10Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.
4Mtima wa anzeru uli m'nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m'nyumba ya kuseka.
5Mas. 141.5Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.
6Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.
7Deut. 16.19Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.
8Miy. 14.29Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.
9Miy. 16.32; Yak. 1.19Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'chifuwa cha zitsiru.
10Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.
11Nzeru ili yabwino pamodzi ndi cholowa; akuona dzuwa apindula nayo.
12Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.
13Yes. 14.27Tapenya ntchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa chomwe iye anachikhotetsa?
14Deut. 28.45-47Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.
15Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m'chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwake.
16Aro. 12.3Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha?
17Mas. 55.23Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?
18Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzatuluka monsemo.
19Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akulu khumi akulamulira m'mzinda.
201Maf. 8.46; Aro. 3.23; 1Yoh. 1Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.
21Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;
22pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.
23 Aro. 1.22 Ndayesa zonsezi ndi nzeru; ndinati, Ndidzakhala wanzeru; koma inanditalikira.
24Chakutali ndi chakuyadi, adzachipeza ndani?
25Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;
26Miy. 5.3-4ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.
27Taonani, ichi ndachipeza, ati Mlalikiyo, m'kuphatikiza chinthu china ndi chinzake, ndikazindikire malongosoledwe ao;
28chomwe moyo wanga uchifuna chifunire, koma osachipezai ndi ichi, mwamuna mmodzi mwa chikwi ndinampezadi, koma mkazitu mwa onsewo sindinampeze.
29Gen. 1.27; 3.6-7Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.