MLALIKI 10 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Kupusa kusautsa kwambiri

1Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.

2Wanzeru, mtima wake uli kudzanja lake lamanja; koma chitsiru, mtima wake kulamanzere.

3Inde, poyendanso chitsiru panjira, nzeru yake imthera ndipo angoti kwa onse kuti, Ndine chitsiru.

41Sam. 25.24-33Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.

5Pali choipa ndachiona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkulu;

6Est. 3.1utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi.

7Miy. 19.10Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akapolo.

8Miy. 26.27Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.

9Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.

10Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza.

11Yer. 8.17Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.

12Luk. 4.22Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga chisomo; koma milomo ya chitsiru idzachimeza.

13Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.

14Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake?

15Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sichidziwa kunka kumzinda.

16Yes. 3.4-5, 12Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa!

17Mwai kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana wa aufulu, ndipo akalonga ako adya pa nthawi yoyenera akalimbe osati akaledzere ai.

18Tsindwi litewa ndi mphwai za eni ake; nyumba nidontha ndi ulesi wa manja.

19Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse.

20Mrk. 6.2-3Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help