1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2Taona ndaitana ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;
31Maf. 7.14ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m'ntchito zilizonse,
4kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golide ndi siliva ndi mkuwa,
5ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kozokota mtengo, kuchita ntchito zilizonse.
6Ndipo Ine, taona, ndampatsa Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m'mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe;
7chihema chokomanako, likasa la mboni, ndi chotetezerapo chili pamwamba pake, ndi zipangizo zonse za chihemacho;
8ndi gomelo ndi zipangizo zake, ndi choikaponyali choona ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo;
9ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake;
10ndi zovala zotumikira nazo, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakuchita nazo ntchito ya nsembe;
11ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe.
Masungidwe a tsiku la Sabata12Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
13Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.
14Eks. 20.8; Ezk. 20.12, 20Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m'mwemo, munthu ameneyo achotsedwe mwa anthu a mtundu wake.
15Num. 15.32-36Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.
16Chifukwa chake ana a Israele azisunga Sabata, kuchita Sabata mwa mibadwo yao, likhale pangano losatha;
17Gen. 2.2-3ndicho chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi ana a Israele; pakuti Yehova analenga kumwamba ndi dziko lapansi m'masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonanso mphamvu.
18Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.