MLALIKI Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaBukuli lipereka maganizo a Mphunzitsi wina amene adayesetsa kumvetsa za moyo wa munthu; poona kuti moyowo sukhalira kutha ndiponso ndi wodzaza ndi mavuto, poonanso kuti zinthu siziyenda motsata chilungamo monga momwe mwini wake ankayembekezera. Mlalikiyo atafufuza zonsezi anagoti, “Zachabechabe…zachabechabe zonse ndi chabe.” Sankamvetsa njira zake za Mulungu, amene amaongolera moyo wa anthu ndi zinthu zina zonse mwa njira yodziwa Iye yekha, potsata zomwe Iye amaganizira pa chiyambi. Komabe Mlalikiyo akuwauza anthu kuti agwire ntchito molimbika ndiponso azikondwerera mphatso za Mulungu mpaka kukhutira pa nthawi yonse ya moyo wao.Mwina anthu sangavomerezane ndi maganizo ambiri a Mlaliki, poona kuti maganizowo ngokayikitsa ndi otayitsa mtima. Komabe popeza kuti bukuli lipezeka mu Baibulo, ndiye kuti ngakhale maganizo amenewa angathe kuthandiza anthu ambiri kumvetsa za m'mene moyo wao uliri, akamasinkhasinkha mau ena ambiri a mu Baibulo momwemo onena za madalitso aakulu amene Mulungu wasungira anthu okhulupirira Iyeyo.Za mkatimuKodi moyo uli ndi cholinga? 1.1—2.26

Zonena zokhudza moyo 3.1—11.8

Malangizo otsiriza 11.9—12.8

Mau omaliza 12.9-14

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help