1 Yer. 10.24 Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,
ndipo musandilange muukali wanu.
2 Mas. 41.4 Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine.
Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
3 Yoh. 12.27 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu;
ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?
4Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;
ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.
5 Mas. 30.9 Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu;
m'mandamo adzakuyamikani ndani?
6Ndalema nako kuusa moyo kwanga;
ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;
mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.
7 Yob. 17.7 Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni;
lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa.
8 Mat. 7.23; 25.41 Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake;
pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.
9Wamva Yehova kupemba kwanga;
Yehova adzalandira pemphero langa.
10Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu
adani anga onse;
adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.