1Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;
2Ower. 2.2nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo.
3Yos. 23.12-13; Ezr. 9.2Ndipo musakwatitsane nao; musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.
4Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.
5Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.
6Yer. 2.3; 1Pet. 2.9Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.
7Yehova sanakondwere nanu, ndi kukusankhani chifukwa cha kuchuluka kwanu koposa mitundu ina yonse ya anthu, kapena kuchepera kwanu;
8Hos. 11.1; Eks. 32.13koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya ukapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.
91Ako. 1.9; 1Ate. 5.24; Aheb. 10.23; 1Yoh. 1.9Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.
10Ndipo awabwezera onse akudana ndi Iye, pamaso pao, kuwaononga; sachedwa naye wakudana ndi Iye, ambwezera pamaso pake.
11Potero muzisunga malamulo, ndi malemba, ndi maweruzo amene ndikuuzani lero kuwachita.
12 Luk. 1.72-73 Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu;
13Yoh. 14.21ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.
14Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu.
15Ndipo Yehova adzakuchotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa zilizonse za Aejipito muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.
16Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.
17Mukadzanena m'mtima mwanu, Amitundu awa andichulukira; ndikhoza bwanji kuwapirikitsa?
18Musamawaopa; mukumbukire bwino chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Farao, ndi Ejipito wonse;
19mayesero aakulu maso anu anawapenya, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakutulutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa.
20Komanso Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pao, kufikira ataonongeka otsalawo, ndi akubisala pamaso panu.
21Yos. 3.10; Neh. 4.14Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.
22Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang'onopang'ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakuchulukireni zilombo.
23Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka pamaso panu, nadzawapirikitsa ndi kupirikitsa kwakukulu, kufikira ataonongeka.
24Yos. 23.9Adzaperekanso mafumu ao m'dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga.
25Yos. 7.1, 21Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.
26Musamalowa nacho chonyansachi m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse; popeza ndi chinthu choyenera kuonongeka konse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.