1 ATESALONIKA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaMzinda wa Tesalonika unali likulu la dziko la Masedoniya lokhala mu ulamuliro wa Aroma. Paulo adayambitsa mpingo kumeneko, atachoka ku Filipi. Koma Ayuda ataona kuti Paulo akulalika uthenga wa Chikhristu kwa anthu a mitundu ina okonda zachiyuda namakopa ambiri mwa iwo, adachita naye dumbo, namadana naye ndi kumvutitsa; mwakuti Paulo adachoka kumeneko kupita ku Bereya. Atafika ku Korinto, Timoteo, mnzake womthandiza pa ntchito yolalikira, adadzampeza namusimbira za m'mene mpingo ukuyendera ku Tesalonika.Paulo anawalembera kalatayi kuti awalimbitse mtima ndi kuyankha mafunso ao, makamaka pa nkhani yokhudza kubweranso kwa Ambuye. Akuwakumbutsa za m'mene iyeyo ankakhalira pakati pao. Akulakalaka kukawayenderanso. Paulo akugwiritsa ntchito mwayiwu kuti awauze za Akhristu amene anamwalira kale, Khristu asanabwere. Kodi nanga Khristuyo adzabweranso liti? Paulo akuwauza kuti akonzekere modekha ndi kuyembekezera kubweranso kwa Ambuye.Za mkatimuMau oyamba 1.1Kuyamikira ndi kuyamika 1.2—3.13Chilimbikitso pa moyo wa Chikhristu wabwino 4.1-12Malangizo pakubweranso kwa Khristu 4.13—5.11Machenjezo omaliza 5.12-22Mau omaliza 5.23-28