YEREMIYA 33 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yehova abwereza kunena kuti anthu ake adzakhazikikanso m'dziko mwao, padzakhalanso mphukira

1 Yer. 32.2 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya nthawi yachiwiri, pamene iye anali chitsekedwere m'bwalo la kaidi, kuti,

2Eks. 6.2-3Atero Yehova wochita zake, Yehova wolenga zake kuti azikhazikitse; dzina lake ndi Yehova:

3Mas. 91.15Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zopambana, zimene suzidziwa.

4Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israele, za nyumba za mzinda uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda'zi, zinagwetsedwa ziwatchinjirizire mitumbira, ndi lupanga:

5Yer. 32.5Adza kumenyana ndi Ababiloni, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mzinda uno nkhope yanga chifukwa cha zoipa zao zonse.

6Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuchiritsa, ndi kuwachiritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona.

7Yer. 32.44Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israele, ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, monga poyamba paja.

8Ezk. 36.25; Mik. 7.18; Aheb. 9.13-14Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.

9Yes. 62.7Ndipo ndidzayesa mzinda uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a padziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.

10Atero Yehova: M'malo muno, m'mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m'mizinda ya Yuda, m'makwalala a Yerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,

11Yer. 25.10mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.

12Yes. 65.10Yehova wa makamu atero: M'malo muno, muli bwinja, mopanda munthu ndi nyama, m'mizinda yake yonse, mudzakhalanso mokhalamo abusa ogonetsa zoweta zao.

13Lev. 27.32; Yoh. 10.14M'mizinda ya kumtunda, m'mizinda ya kuchidikha, m'mizinda ya kumwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'mizinda ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.

14Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzakhazikitsa mau abwino aja ndinanena za nyumba ya Israele ndi za nyumba ya Yuda.

15Yes. 4.2; 11.1Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukutsira Davide mphukira ya chilungamo; ndipo adzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dzikomu.

16Yer. 23.6Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzatchedwa nalo, Yehova ndiye chilungamo chathu.

171Maf. 2.4Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wachifumu wa nyumba ya Israele;

18Aro. 12.1; 1Pet. 2.5, 9ndiponso ansembe a fuko la Levi sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakuchita nsembe masiku onse.

19Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

20Mas. 89.35-37Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m'nyengo yao;

21pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.

22Gen. 13.16; 22.17Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.

23Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

24Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.

25Gen. 8.22Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;

26Yer. 33.7, 11pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help