1Mulungu adziwika mwa Yuda,
dzina lake limveka mwa Israele.
2 Gen. 14.18 Msasa wake unali mu Salemu,
ndipo pokhala Iye mu Ziyoni.
3 Ezk. 39.9 Pomwepo anathyola mivi ya pauta;
chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.
4Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka
wakuposa mapiri muli achifwamba.
5Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao;
amuna onse amphamvu asowa manja ao.
6 Eks. 15.1, 21 Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo,
galeta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo.
7 Nah. 1.6 Inu ndinu woopsa;
ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu?
8 Ezk. 38.19-20 Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba;
dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete,
9pakuuka Mulungu kuti aweruze,
kuti apulumutse ofatsa onse a padziko lapansi.
10 Eks. 9.16 Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani;
chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.
11 Mas. 50.14 Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;
onse akumzinga abwere nacho chopereka
cha kwa Iye amene ayenera kumuopa.
12Iye adzadula mzimu wa akulu;
akhala woopsa kwa mafumu a padziko lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.