1 1Mbi. 6.31, 33, 39 Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi chiwerengo cha antchito monga mwa kutumikira kwao ndicho:
2a ana a Asafu: Zakuri, ndi Yosefe, ndi Netaniya, ndi Asarela, ana a Asafu; mwa chilangizo cha Asafu, wakunenera mwa chilangizo cha mfumu.
3A Yedutuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa chilangizo cha atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.
4A Hemani, ana a Hemani: Bukiya, Mataniya, Uziyele, Sebuele, ndi Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, ndi Romamiti-Ezere, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, Mahaziyoti;
5awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m'mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yake. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna khumi ndi anai, ndi ana aakazi atatu.
6Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
7Ndipo chiwerengo chao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa aimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.
8Lev. 16.8; 1Mbi. 26.13Ndipo anachita maere pa udikiro wao, analingana onse, ang'ono ndi akulu, mphunzitsi ndi wophunzira.
9Maere oyamba tsono anagwera a banja la Asafu ndiye Yosefe; wachiwiri Gedaliya, iye ndi abale ake, ndi ana ake khumi ndi awiri;
10wachitatu Zakuri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
11wachinai Iziri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
12wachisanu Netaniya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
13wachisanu ndi chimodzi Bukiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
14wachisanu ndi chiwiri Yesarela, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
15wachisanu ndi chitatu Yesaya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
16wachisanu ndi chinai Mataniya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
17wakhumi Simei, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
18wakhumi ndi chimodzi Azarele, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
19wakhumi ndi chiwiri Hasabiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
20wakhumi ndi chitatu Subaele, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
21wakhumi ndi chinai Matitiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
22wakhumi ndi chisanu Yeremoti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
23wakhumi ndi chisanu ndi chimodzi Hananiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
24wakhumi ndi chisanu ndi chiwiri Yosibekasa, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
25wakhumi ndi chisanu ndi chitatu Hanani, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
26wakhumi ndi chisanu ndi chinai Maloti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
27wamakumi awiri Eliyata, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
28wa makumi awiri ndi chimodzi Hotiri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
29wa makumi awiri ndi chiwiri Gidaliti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
30wa makumi awiri ndi chitatu Mahaziyoti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;
31wa makumi awiri ndi chinai Romamiti-Ezere, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.