MASALIMO 138 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide ayamika Mulungu pa kukhulupirika kwake, naneneratu kuti mafumu onse adzateroSalimo la Davide.

1Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse;

ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.

2 1Maf. 8.28, 30; Yes. 42.21 Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera,

ndi kuyamika dzina lanu,

chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu;

popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.

3Tsiku loitana ine, munandiyankha,

munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.

4 Mas. 102.15, 22 Mafumu onse a padziko lapansi adzakuyamikani,

Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.

5Ndipo adzaimbira njira za Yehova;

pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

6 Yak. 4.6 Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo;

koma wodzikuza amdziwira kutali.

7 Mas. 23.3-4 Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo;

mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu,

ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.

8 Afi. 1.6 Yehova adzanditsirizira za kwa ine:

Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse:

Musasiye ntchito za manja anu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help