1Tikuyamikani Inu, Mulungu;
tiyamika, pakuti dzina lanu lili pafupi;
afotokozera zodabwitsa zanu.
2Pakuona nyengo yake ndidzaweruza molunjika.
3Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo;
ndinachirika mizati yake.
4Ndinati kwa odzitamandira,
musamachita zodzitamandira;
ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;
5musamakwezetsa nyanga yanu;
musamalankhula ndi khosi louma.
6Pakuti kukuzaku sikuchokera kum'mawa,
kapena kumadzulo, kapena kuchipululu.
7 Mas. 50.6; 1Sam. 2.7 Pakuti Mulungu ndiye woweruza;
achepsa wina, nakuza wina.
8 Mas. 60.3 Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho;
ndi vinyo wake achita thovu;
chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako.
Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa
nadzagugudiza nsenga zake.
9Koma ine ndidzalalikira kosalekeza,
ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo.
10 Mas. 89.17; Yer. 48.25 Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa;
koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.