1 1Maf. 12.21-24 Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehobowamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisraele kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu.
2Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti,
3Lankhula ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,
4Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense kunyumba yake; pakuti chinthu ichi chifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobowamu.
5Ndipo Rehobowamu anakhala mu Yerusalemu, namanga mizinda yolimbikiramo mu Yuda.
6Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekowa,
7ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,
8ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,
9ndi Adoraimu, ndi Lakisi, ndi Azeka,
10ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo mizinda yamalinga ya mu Yuda ndi Benjamini.
11Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi chakudya chosungikiratu, ndi mafuta, ndi vinyo.
12Ndi m'mizinda iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake.
Alevi ndi Aisraele ambiri afika ku Yerusalemu13Ndipo ansembe ndi Alevi okhala mu Israele yense anadziphatikiza kwa iye, ochokera m'malire ao onse.
14Num. 35.2; 2Mbi. 13.9Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;
151Maf. 12.28, 31; 13.33nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a anaang'ombe adawapanga.
162Mbi. 15.9Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.
172Mbi. 12.1Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehobowamu, mwana wa Solomoni zaka zitatu; pakuti anayenda m'njira ya Davide ndi Solomoni zaka zitatu.
18Ndipo Rehobowamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu mwana wa Yese;
19ndipo anambalira ana, Yeusi, ndi Semariya, ndi Zahamu.
20Ndi pambuyo pake anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti.
21Ndipo Rehobowamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ake onse, ndi akazi ake aang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana aamuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana aakazi makumi asanu ndi limodzi).
22Ndipo Rehobowamu anaika Abiya mwana wa Maaka akhale wamkulu, kalonga mwa abale ake; ndiko kuti adzamlonga ufumu.
23Ndipo anachita mwanzeru, nabalalitsa ana ake aamuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, kumizinda yonse yamalinga; nawapatsa chakudya chochuluka, nawafunira akazi ochuluka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.