1 MBIRI 8 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Adzukulu a Benjamini ndi Saulo

1Ndipo Benjamini anabala Bela mwana wake woyamba, Asibele wachiwiri, ndi Ahara wachitatu,

2Noha wachinai, ndi Rafa wachisanu.

3Ndi Bela anali ndi ana: Adara, ndi Gera, ndi Abihudi,

4ndi Abisuwa, ndi Naamani, ndi Ahowa,

5ndi Gera, ndi Sefufani, ndi Huramu.

6Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akulu a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kunka ku Manahati,

7natenga ndende Naamani, ndi Ahiya, ndi Gera, ndipo, anabala Uza, ndi Ahihudi.

8Ndipo Saharaimu anabala ana ku dziko la Mowabu, atachotsa akazi ake Husimu ndi Baara.

9Ndipo Hodesi mkazi wake anambalira Yobabu, ndi Zibiya, ndi Mesa, ndi Malikamu,

10ndi Yeuzi, ndi Sakiya, ndi Mirima. Awa ndi ana ake aakulu a nyumba za makolo ao.

11Ndi Husimu anambalira Abitubu, ndi Elipaala.

12Ndi ana a Elipaala: Eberi, ndi Misamu, ndi Semedi, amene anamanga Ono, ndi Lodi ndi midzi yake,

13ndi Beriya, ndi Sema; ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo okhala mu Ayaloni, amene anathawitsa okhala mu Gati;

14ndi Ahiyo, Sasaki, ndi Yeremoti,

15ndi Zebadiya, ndi Aradi, ndi Edere,

16ndi Mikaele, ndi Isipa, ndi Yoha, ana a Beriya;

17ndi Zebadiya, ndi Mesulamu, ndi Hiziki, ndi Hebere,

18ndi Isimerai, ndi Iziliya, ndi Yobabu, ana a Elipaala;

19ndi Yakimu, ndi Zikiri, ndi Zabidi,

20ndi Eliyenai, ndi Ziletai, ndi Eliyele,

21ndi Adaya, ndi Beraya, ndi Simiratu, ana a Simei;

22ndi Isipani, ndi Eberi, ndi Eliyele,

23ndi Abidoni, ndi Zikiri, ndi Hanani,

24ndi Hananiya, ndi Elamu, ndi Antotiya,

25ndi Ifidea, ndi Penuwele, ana a Sasaki;

26ndi Samuserai, ndi Sehariya, ndi Ataliya,

27ndi Yaaresiya ndi Eliya, ndi Zikiri, ana a Yerohamu.

28Awa ndi akulu a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akulu anakhala mu Yerusalemu awa.

29Ndipo mu Gibiyoni anakhala atate a Gibiyoni, dzina la mkazi wake ndiye Maaka;

30ndi mwana wake woyamba ndiye Abidoni, opondana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Nadabu,

31ndi Gedori, ndi Ahiyo, ndi Zekeri.

32Ndipo Mikiloti anabala Simea. Ndi iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao mu Yerusalemu, popenyana ndi abale ao.

331Sam. 14.51Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.

34Ndi mwana wa Yonatani, ndiye Meribaala; ndi Meribaala anabala Mika.

35Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi.

36Ndi Ahazi anabala Yehoyada, ndi Yehoyada anabala Alemeti, ndi Azimaveti, ndi Zimiri; ndi Zimiri anabala Moza;

37ndi Moza anabala Bineya, mwana wake ndiye Rafa, mwana wake Eleasa, mwana wake Azele;

38ndipo Azele anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndiwo Azirikamu, Bokeru, ndi Ismaele, ndi Seyariya, ndi Obadiya, ndi Hanani. Onsewa ndiwo ana a Azele.

39Ndipo ana a Eseki mbale wake: Ulamu mwana wake woyamba, Yeusi wachiwiri, ndi Elifeleti wachitatu.

40Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mivi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help