AGALATIYA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaPamene uthenga wabwino wonena za Yesu unayamba kulalikidwa ndi kulandiridwa pakati pa anthu amene sanali Ayuda, funso lalikulu limene limafunsidwa linali lakuti: Kodi ndikoyenera kuti munthu atsatire Malamulo a Mose ngati akufuna kukhala Mkhristu? Paulo ananena kuti izi sizinali zoyenera. Iye anatinso chofunika pa moyo wotsatira Khristu ndi ndicho chakuti anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu pokhulupirira Khristu basi. Komabe pakati pa mipingo ya ku Galatiya, limene linali dera la ku Asiya, panali anthu amene anabwera ndi kumasutsana ndi Paulo ponena kuti munthu ayenera kutsata Malamulo a Mose ngati akufuna alungamitsidwe ndi Mulungu. Kalata ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Agalatiya inalembedwa pofuna kukonza chiphunzitso cholakwikachi chimene ena anabweretsa ndi kupotoza nacho anthu anzao. Paulo anayamba pa kuteteza udindo wake monga mtumwi wa Yesu Khristu. Iye anatsindika mfundo yakuti maitanidwe ake kukhala mtumwi anachokera kwa Mulungu, osati kwa munthu, ndiponso kuti utumiki wake unali wa kwa anthu sanali Ayuda. Kenaka akufotokoza kuti anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu pokhapokha pamene akhulupirira. Mu mitu yomalizira, Paulo akutionetsa kuti khalidwe labwino la Chikhristu limachokera ku chikondi chimene chimapezeka pamene munthu wakhulupirira Yesu.Za mkatimuMau oyamba 1.1-10Ulamuliro wa Paulo pokhala mtumwi 1.11—2.21Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu 3.1—4.31Ufulu ndi udindo wa Mkhristu 5.1—6.10Mau omaliza 6.11-18
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help