1 Mas. 96.10 Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere;
zisumbu zambiri zikondwerere.
2 1Maf. 8.12; Mas. 89.14 Pomzinga pali mitambo ndi mdima;
chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa
mpando wake wachifumu.
3 Luk. 1.5, 55, 72 Moto umtsogolera,
nupsereza otsutsana naye pozungulirapo.
4Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu;
dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.
5 Nah. 1.5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,
pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
6 Mas. 19.1 Kumwamba kulalikira chilungamo chake,
ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake.
7 Yes. 42.17 Onse akutumikira fano losema,
akudzitamandira nao mafano, achite manyazi:
Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.
8 Ziyoni anamva nakondwera,
nasekerera ana aakazi a Yuda;
chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.
9 Eks. 18.11 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi,
ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.
10 Mas. 37.28; Amo. 5.15 Inu okonda Yehova, danani nacho choipa:
Iye asunga moyo wa okondedwa ake;
awalanditsa m'manja mwa oipa.
11 Miy. 4.18 Kuunika kufesekera wolungama,
ndi chikondwerero oongoka mtima.
12 Mas. 30.4; 32.11 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;
ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.