HOSEYA 7 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Kuchimwa ndi kupandukira kwa Israele

1M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo.

2Mas. 90.8; Yer. 17.1Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.

3Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao.

4Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wootcha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.

5Tsiku la mfumu yathu akalonga adzidwalitsa ndi kutentha kwa vinyo; iye anatambasula dzanja lake pamodzi ndi oseka.

6Pakuti asendera nao mtima wao wakunga ng'anjo ya mkate, pokhala alikulalira; wootcha mkate wao agona usiku wonse, m'mawa iyaka ngati moto wa malawi.

7Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine.

8Mas. 106.35Efuremu asokonezana nayo mitundu ya anthu; Efuremu ndiye kamtanda ka mkate kosatembenuzidwa.

9Alendo anatha mphamvu yake osachidziwa iye; imvi zomwe zampakiza osachidziwa iye.

10Ndipo kudzikuza kwa Israele kumchitira umboni pamaso pake; koma sanabwerere kunka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ichi chonse.

112Maf. 15.19; 17.4; Hos. 11.11Ndipo Efuremu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Ejipito, amuka kwa Asiriya.

12Pamene amuka ndidzawayalira ukonde wanga, ndidzawagwetsa ngati mbalame za m'mlengalenga, ndidzawalanga monga udamva msonkhano wao.

13Mik. 6.4Tsoka kwa iwowa! Pakuti anandizembera; chionongeko kwa iwowa! Pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza.

14Yer. 3.10Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.

15Chinkana ndawalangiza ndi lulimbitsa manja ao, andilingiririra choipa.

16Mas. 78.57Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help