1 Ezk. 6.2 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, unenere kwa mapiri a Israele, uziti, Mapiri a Israele inu, imvani mau a Yehova.
2Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Ha! Ingakhale misanje yakale ili yathu, cholowa chathu;
31Maf. 9.7chifukwa chake unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Chifukwa, inde chifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale cholowa cha amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;
4chifukwa chake, mapiri inu a Israele, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi mizinda yamabwinja, imene yakhala chakudya ndi choseketsa amitundu otsala akuzungulira;
5Deut. 4.24chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu yense, amene anadzipatsira dziko langa likhale cholowa chao ndi chimwemwe cha mtima wonse, ndi mtima wopeputsa, kuti alande zake zonse zikhale zofunkha.
6Mas. 123.3-4Chifukwa chake unenere za dziko la Israele, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu;
7chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndakweza dzanja langa Ine, ndi kuti, Zedi amitundu akuzungulira inu adzasenza manyazi ao.
8Koma inu, mapiri a Israele, mudzaphukitsa nthambi zanu, ndi kubalira anthu anga Israele zipatso zanu, pakuti ayandikira kufika.
9Pakuti taonani, Ine ndikhalira nanu kumodzi, ndipo ndidzakutembenukirani; ndipo mudzabzalidwa ndi kupaliridwa,
10Amo. 9.14ndipo ndidzakuchulukitsirani anthu nyumba yonse ya Israele, yonseyi, ndi m'mizindamo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa mizinda.
11Yer. 31.27Ndipo ndidzakuchulukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzachuluka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzachitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
12Oba. 17-21Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israele; adzakhala nawe dziko laolao, ndipo udzakhala cholowa chao osafetsanso ana ao.
13Num. 13.32Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa;
14chifukwa chake sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso a mtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova.
15Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzasenzanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.
Za kukonzekanso kwa Israele16Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,
17Lev. 18.25-28Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israele anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi machitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga chidetso cha mkazi amene akusamba.
18M'mwemo ndinawatsanulira ukali wanga, chifukwa cha mwazi anautsanulira padziko, ndi chifukwa cha mafano analidetsa nalo dziko;
19Ezk. 39.24ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m'maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa machitidwe ao ndinawaweruza.
20Aro. 2.24Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, natuluka m'dziko mwake.
21Koma ndinawaleka chifukwa cha dzina langa loyera, limene a nyumba ya Israele adalidetsa pakati pa amitundu, kumene adankako.
22Mas. 106.8Chifukwa chake nena kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Sindichichita ichi chifukwa cha inu, nyumba ya Israele, koma chifukwa cha dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.
23Ezk. 20.41Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikulu kuti lili loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao.
24Ezk. 37.21Pakuti ndidzakutengani kukutulutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m'maiko onse, ndi kubwera nanu m'dziko lanu.
25Yes. 52.15; Yer. 33.8; Aheb. 10.22Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.
26Ezk. 11.19-20Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.
27Ezk. 11.19-20Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.
28Yer. 30.22; Ezk. 11.19-20Ndipo mudzakhala m'dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu.
29Aro. 11.26Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumchulukitsa, osaikiranso inu njala.
30Ndipo ndidzachulukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m'munda, kuti musalandirenso chitonzo cha njala mwa amitundu.
31Ezk. 16.61, 63Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.
32Deut. 9.5; Ezk. 36.22Dziwani kuti sindichita ichi chifukwa cha inu, ati Ambuye Yehova; chitani manyazi, dodomani, chifukwa cha njira zanu, nyumba ya Israele inu.
33Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukuchotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m'mizindamo; ndi pamabwinja padzamangidwa.
34Ndi dziko lachipululu lidzalimidwa, chinkana linali lachipululu pamaso pa onse opitako.
35Ndipo adzati, Dziko ili lachipululu lasanduka ngati munda wa Edeni ndi mizinda yamabwinja, ndi yachipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m'mwemo.
36Ezk. 37.14Pamenepo amitundu otsala pozungulira panu adzadziwa kuti Ine Yehova ndamanga malo opasuka, ndi kubzala pamene panali chipululu; Ine Yehova ndanena ndidzachita.
37 Ezk. 20.3, 31 Atero Ambuye Yehova, Ichi chomwe adzandipempha a nyumba ya Israele ndiwachitire ichi, ndidzawachulukitsira anthu ngati nkhosa.
38Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa zikondwerero zake zoikika, momwemo mizinda yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.