1 2Maf. 18.17 Chaka chimene kazembe wa ku Asiriya anafika ku Asidodi, muja Sarigoni mfumu ya Asiriya anamtumiza iye, ndipo iye anamenyana ndi Asidodi, naugonjetsa.
21Sam. 19.24; Zek. 13.4Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule chiguduli m'chuuno mwako, nuchichotse, nuvule nsapato yako kuphazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda maliseche, ndi wopanda nsapato.
3Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale chizindikiro ndi chodabwitsa kwa Ejipito ndi kwa Etiopiya;
4momwemo mfumu ya Asiriya idzatsogolera kwina am'nsinga a Ejipito, ndi opirikitsidwa a Etiopiya, ana ndi okalamba, amaliseche ndi opanda nsapato, ndi matako osavala, kuti achititse manyazi Ejipito.
5Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, chifukwa cha Kusi, amene anawatama, ndi Ejipito, amene anawanyadira.
6Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asiriya, ndipo ife tidzapulumuka bwanji?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.