1 Agal. 1.11-12 Paulo, mtumwi (wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa),
2ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwa Mipingo ya ku Galatiya:
3Chisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu,
4Mat. 20.28; Yoh. 17.14-15amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano ino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu;
5yemweyo akhale nao ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
Kupatuka kwa Agalatiya. Utumiki wa Paulo uchokera kwa Mulungu6 Agal. 5.8 Ndizizwa kuti msanga motere mulikupatuka kwa iye amene anakuitanani m'chisomo cha Khristu, kutsata Uthenga Wabwino wina;
7Mac. 15.1, 24umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.
81Ako. 16.22Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni Uthenga Wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.
91Ako. 16.22Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani Uthenga Wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.
101Ate. 2.4Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.
11 1Ako. 15.1-3 Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.
121Ako. 15.1-3; Aef. 3.3; Agal. 1.1Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa vumbulutso la Yesu Khristu.
13Mac. 22.4Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Chiyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,
14Mac. 22.3ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.
15Yes. 49.1, 5; Mac. 9.15Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake,
16Mac. 9.15; 2Ako. 4.6; Aef. 3.8kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsane ndi thupi ndi mwazi:
17kapena kukwera kunka ku Yerusalemu sindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.
18Mac. 9.26Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.
19Koma wina wa atumwi sindinamuone, koma Yakobo mbale wa Ambuye.
20Aro. 9.1Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.
21Mac. 9.30Pamene ndinadza kumbali za Siriya ndi Silisiya.
221Ate. 2.14Koma ndinali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Khristu;
23koma analinkumva kokha, kuti, Iye wakutilondalonda ife kale, tsopano alalikira chikhulupirirocho adachipasula kale;
24ndipo analemekeza Mulungu mwa ine.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.