1 Mas. 103.1 Aleluya;
Ulemekeze Yehova, moyo wanga.
2 Mas. 104.33 Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga;
ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.
3 Mas. 118.8-9; Yes. 2.22 Musamakhulupirira zinduna,
kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.
4 Nah. 1.7 Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake;
tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.
5 Yer. 17.7 Wodala munthu amene akhala naye
Mulungu wa Yakobo kuti amthandize,
chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
6Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi,
nyanja ndi zonse zili m'mwemo.
Ndiye wakusunga choonadi kosatha,
7 Mas. 103.6; Yes. 61.1 ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika;
ndiye wakupatsa anjala chakudya;
Yehova amasula akaidi.
8 Mat. 9.30; Luk. 13.12-13; Yoh. 9.7-32 Yehova apenyetsa osaona;
Yehova aongoletsa onse owerama;
Yehova akonda olungama.
9 Deut. 10.18 Yehova asunga alendo;
agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye;
koma akhotetsa njira ya oipa.
10 Eks. 15.18; Chiv. 11.15 Yehova adzachita ufumu kosatha,
Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo.
Aleluya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.