1 1Ako. 10.12; 2Ate. 3.15 Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.
2Aro. 15.1Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.
3Aro. 12.3Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.
42Ako. 13.5Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.
51Ako. 3.8Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.
6Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.
7Luk. 16.25Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.
8Aro. 8.13Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.
91Ako. 15.58Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.
101Ate. 5.15Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
11Taonani, malembedwe aakuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini.
12Agal. 5.11Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu.
13Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu.
14Aro. 6.6; Afi. 3.3, 7-8Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.
15Agal. 5.6; Akol. 3.11Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.
16Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu.
172Ako. 11.23Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu.
18Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.