MLALIKI 9 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Okoma ndi oipa amamva zomwezo. Khalani nazo zakupatsa Mulungu mokondwera

1Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi ntchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse zili m'tsogolo mwao.

2Mas. 73.3, 12-13Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira.

3Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.

4Pakuti woyang'ana ndi amoyo onse ali nacho chiyembekezo; pakuti galu wamoyo aposa mkango wakufa.

5Yes. 26.14Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.

6Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kalikonse kachitidwe pansi pano.

7Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.

8Chiv. 3.4Zovala zako zikhale zoyera masiku onse; mutu wako usasowe mafuta.

9Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.

10Aro. 12.11Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.

Nzeru ya mwini ilanditsa ena

11 Amo. 2.14-15; Yer. 9.23 Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.

12Luk. 12.20, 39; 1Ate. 5.3Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.

13Ndaonanso nzeru pansi pano motero, ndipo inandionekera yaikulu;

14panali mzinda waung'ono muli anthu owerengeka; ndipo inadzako mfumu yaikulu, nawuzinga ndi nkhondo, nkumanga malinga aakulu;

15koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mzindawo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.

16Eks. 22.28; Miy. 21.22; Mac. 23.5Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.

17Mau a anzeru achete amveka koposa kufuula kwa wolamulira mwa zitsiru.

18Yos. 7.1, 11-12Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help