1 Miy. 29.3, 15 Mwana wanzeru akondweretsa atate;
koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.
2 Dan. 4.27; Luk. 12.19 Chuma cha uchimo sichithangata;
koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.
3 Mas. 34.9-10 Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama;
koma amainga chifuniro cha wochimwa.
4Wochita ndi dzanja laulesi amasauka;
koma dzanja la akhama lilemeretsa.
5Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru;
koma wogona pakututa ndi mwana wochititsa manyazi.
6Madalitso ali pamutu pa wolungama;
koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.
7 Mas. 9.5-6; 112.6 Amayesa wolungama wodala pomkumbukira;
koma dzina la oipa lidzavunda.
8Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo;
koma chitsiru cholongolola chidzagwa.
9 Yes. 33.15-16 Woyenda moongoka amayenda osatekeseka;
koma wokhotetsa njira zake adzadziwika.
10Wotsinzinira achititsa chisoni;
koma wodzudzula momveka achita mtendere.
11 Mas. 37.30 M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo;
koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.
12 1Ako. 13.4; 1Pet. 4.8 Udani upikisanitsa;
koma chikondi chikwirira zolakwa zonse.
13Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira;
koma wopusa pamsana pake nthyole.
14Anzeru akundika zomwe adziwa;
koma m'kamwa mwa chitsiru muononga tsopano lino.
15 Mas. 52.7; 1Tim. 6.17 Chuma cha wolemera ndi mzinda wake wolimba;
koma umphawi wao uononga osauka.
16Ntchito za wolungama zipatsa moyo;
koma phindu la oipa lichimwitsa.
17Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo;
koma wosiya chidzudzulo asochera.
18 Mas. 15.3 Wobisa udani ali ndi milomo yonama;
wonena ugogodi ndiye chitsiru.
19 Yak. 3.2 Pochuluka mau zolakwa sizisoweka;
koma wokhala chete achita mwanzeru.
20Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika;
koma mtima wa oipa uli wachabe.
21Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;
koma zitsiru zimafa posowa nzeru.
22 Gen. 24.35 Madalitso a Yehova alemeretsa,
saonjezerapo chisoni.
23Masewero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa;
koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.
24 1Yoh. 5.14-15 Chomwe woipa achiopa chidzamfikira;
koma chomwe olungama achifuna chidzapatsidwa.
25 Mat. 7.24 Monga kavumvulu angopita, momwemo woipa kuli zii;
koma olungama ndiwo maziko osatha.
26Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso,
momwemo waulesi kwa iwo amene amtuma.
27 Mas. 55.23 Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;
koma zaka za oipa zidzafinimpha.
28 Mas. 112.10 Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe;
koma chidikiro cha oipa chidzaonongeka.
29Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima;
koma akuchita zoipa adzaonongeka.
30 Mas. 125.1 Wolungama sadzachotsedwa konse;
koma oipa sadzakhalabe m'dziko.
31M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru;
koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32 Mas. 37.30 Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa;
koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.