DEUTERONOMO 19 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Za mizinda yopulumukirako(Num. 35.9-34; Yos. 20.1-9)

1Pamene Yehova Mulungu wanu ataononga amitundu, amene Yehova Mulungu wanu akupatsani dziko lao, ndipo mutalilandira lanulanu, ndi kukhala m'mizinda mwao, ndi m'nyumba zao;

2Num. 35.10-11pamenepo mudzipatulire mizinda itatu pakati padziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.

3Mudzikonzere njira, ndi kugawa malire a dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu, patatu; kuti wakupha munthu athawireko.

4Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzake wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzake osati dala, osamuda kale lonse;

5monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzake kutema mitengo, ndi dzanja lake liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguluka m'mpinimo, nikomana ndi mnzake, nafa nayo; athawire ku wina wa mizinda iyi, kuti akhale ndi moyo;

6kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzake, pokhala mtima wake watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanapalamule imfa, poona sanamude kale lonse.

7Chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Mudzipatulire mizinda itatu.

8Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili;

9Yos. 20.7-8ukadzasunga lamulo ili lonse kulichita, limene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake masiku onse; pamenepo mudzionjezere mizinda itatu ina pamodzi ndi itatu iyi;

10kuti angakhetse mwazi wosachimwa pakati padziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, pangakhale mwazi pa inu.

11Koma munthu akamuda mnzake, namlalira, ndi kumuukira ndi kumkantha moyo wake, kuti wafa; nakathawira ku wina wa mizinda iyi;

12pamenepo akulu a mzinda wake atumize ndi kumtengako ndi kumpereka m'manja mwa wolipsa mwazi, kuti afe.

13Num. 35.33Diso lanu lisamchitire chifundo, koma muchotse mwazi wosachimwa mu Israele, kuti chikukomereni.

Za kusendeza malire, ndi za mboni yonama

14 Deut. 27.17; Miy. 22.28 Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'cholowa chanu mudzalandirachi, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.

15 Deut. 17.6 Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.

16Mas. 27.12; Miy. 19.5, 9Mboni yachiwawa ikaukira munthu kumneneza ndi kuti analakwa;

17pamenepo anthu onse awiri, pakati pao pali makaniwo, aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza okhala m'masiku awa;

18ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wake;

19mumchitire monga iye anayesa kumchitira mbale wake; motero muchotse choipacho pakati panu.

20Ndipo otsalawo adzamva, nadzaopa, ndi kusachitanso monga choipacho pakati panu.

21Eks. 21.23-24; Deut. 19.13Ndipo diso lanu lisachite chifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help