MASALIMO 61 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Poopsedwa Davide athamangira MulunguKwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Davide.

1Imvani mfuu wanga, Mulungu;

mverani pemphero langa.

2Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu,

pomizika mtima wanga.

Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.

3 Miy. 18.10 Pakuti munakhala pothawirapo panga;

nsanja yolimba pothawa mdani ine.

4 Mas. 57.1 Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu;

ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.

5Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga;

munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu.

6Mudzatalikitsa moyo wa mfumu.

Zaka zake zidzafikira mibadwomibadwo.

7 Miy. 20.28 Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu;

mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge.

8Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse,

kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help