1 Eks. 25.22 Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;
Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
2Yehova ndiye wamkulu mu Ziyoni;
ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3 Deut. 28.58 Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa.
Ili ndilo loyera.
4 Yes. 61.8 Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo;
Inu mukhazikitsa zolunjika,
muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.
5 1Mbi. 28.2 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,
ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake:
Iye ndiye Woyera.
6 Eks. 14.15; 1Sam. 7.9 Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni,
ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake;
anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
7 Eks. 33.9 Iye analankhula nao mu mtambo woti njo:
Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.
8 Num. 14.20 Munawayankha, Yehova Mulungu wathu:
munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira,
mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.
9 Yes. 6.3 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,
ndipo gwadirani paphiri lake loyera;
pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.