MARKO 15 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yesu aweruzidwa ndi Pilato(Mat. 27.1-2, 11-31; Luk. 23.1-25; Yoh. 18.28—19.16)

1

29Mas. 22.7; Mrk. 14.58; Yoh. 2.19Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu,

30udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda.

31Moteronso ansembe aakulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sangathe kudzipulumutsa yekha.

32Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.

Yesu afa pamtanda(Mat. 27.45-56; Luk. 23.44-49; Yoh. 19.28-30)

33 Luk. 23.44-49 Ndipo pofika ora lachisanu ndi chimodzi, panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.

34Mas. 22.1Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika,

Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?

35Ndipo ena akuimirirapo, pakumva, ananena, Taonani, aitana Eliya.

36Mas. 69.21Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa.

37Ndipo Yesu anatulutsa mau okweza, napereka mzimu wake.

38Luk. 23.44-49Ndipo chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi.

39Luk. 23.44-49Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.

40Mas. 38.11; Mrk. 16.1; Luk. 23.44-49Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yosefe, ndi Salome;

41Luk. 8.2-3amene anamtsata Iye, pamene anali mu Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.

Yesu aikidwa m'manda(Mat. 27.57-66; Luk. 23.50-56; Yoh. 19.38-42)

42Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo pa Sabata,

43Luk. 2.25, 38anadzapo Yosefe wa ku Arimatea, mkulu wa milandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wake wa Yesu.

44Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.

45Ndipo pamene anachidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe mtembowo.

46Luk. 23.53Ndipo anagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m'bafutamo, namuika m'manda osemedwa m'thanthwe; nakunkhunizira mwala pakhomo la manda.

47Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help