1 Gen. 13.8; Aheb. 13.1 Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu
kuti abale akhale pamodzi!
2 Eks. 30.25, 30 Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu,
akutsikira kundevu,
inde kundevu za Aroni;
akutsikira kumkawo wa zovala zake.
3 Deut. 28.8 Ngati mame a ku Heremoni,
akutsikira pa mapiri a Ziyoni.
Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo,
ndilo moyo womka muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.