1Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,
2Tamverani mau anga, inu anzeru;
munditcherere khutu inu akudziwa.
3Pakuti khutu liyesa mau,
monga m'kamwa mulawa chakudya.
4Tidzisankhire choyeneracho,
tidziwe mwa tokha chokomacho.
5 Yob. 29.14 Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama,
ndipo Mulungu wandichotsera choyenera ine
6Kodi ndidzinamizire?
Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwe.
7Wakunga Yobu ndani,
wakumwa mwano ngati madzi?
8Wakutsagana nao ochita mphulupulu,
nayendayenda nao anthu oipa.
9 Yob. 9.22, 23, 30 Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako
kuvomerezana naye Mulungu.
10 Gen. 18.25; Aro. 9.14 Chifukwa chake mundimvere ine, eni nzeru inu,
nkutali ndi Mulungu kuchita choipa,
ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.
11 Mas. 62.12; Mat. 16.27; 2Ako. 5.10 Pakuti ambwezera munthu monga mwa ntchito yake,
napezetsa munthu aliyense monga mwa mayendedwe ake.
12Ndithu zoonadi, Mulungu sangachite choipa,
ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.
13Anamuikiza dziko lapansi ndani?
Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani?
14Akadzikumbukira yekha mumtima mwake,
akadzisonkhanitsira yekha mzimu wake ndi mpweya wake,
15 Gen. 3.19; Yob. 10.9 zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi,
ndi munthu adzabwerera kufumbi.
16Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ichi,
Tcherera khutu kunena kwanga.
17Kodi munthu woipidwa nacho chiweruzo adzalamulira?
Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?
18Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pake iwe,
kapena kwa akalonga, Oipa inu?
19 Deut. 10.17; 2Mbi. 19.7; Mac. 10.34; Aro. 2.11; Aef. 6.9 Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga,
wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka?
Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
20M'kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku,
anthu agwedezeka, napita,
amphamvu achotsedwa opanda dzanja lakuwachotsa.
21 Yob. 31.4 Pakuti maso ake ali panjira ya munthu aliyense,
napenya moponda mwake monse.
22 Mas. 139.12 Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa,
kuti ochita zopanda pake abisaleko.
23Pakuti Mulungu alibe chifukwa cha kulingiriranso za munthu,
kuti afike kwa Iye kudzaweruzidwa.
24Aphwanya eni mphamvu osatulutsa kubwalo mlandu wao,
naika ena m'malo mwao.
25Pakuti asamalira ntchito zao,
nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.
26Awakantha ngati oipa,
poyera pamaso pa anthu,
27popeza anapatuka, naleka kumtsata,
osasamalira njira zake zilizonse.
28 Yak. 5.4 M'mwemo anafikitsa kwa Iye kufuula kwa osauka;
ndipo anamva Iye kufuula kwa ozunzika.
29Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani?
Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani?
Chikachitika pa mtundu wa anthu,
kapena pa munthu, nchimodzimodzi;
30kuti munthu wonyoza Mulungu asachite ufumu,
ndi anthu asakodwe mumsampha.
31Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu,
ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwe?
32Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu,
ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.
33Kodi chilango cha Mulungu chikhale
monga muchifuna inu, pakuti muchikana?
Musankhe ndi inu, ine ai;
m'mwemo monga mudziwa, nenani.
34Anthu ozindikira adzanena nane,
inde anthu anzeru onse akundimva adzati,
35Yobu alankhula wopanda kudziwa,
ndi mau ake alibe nzeru.
36Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha,
chifukwa cha kuyankha kwake monga anthu amphulupulu.
37Pakuti pa kuchimwa kwake aonjeza kupikisana ndi Mulungu,
asansa manja pakati pa ife,
nachulukitsa maneno ake pa Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.