NUMERI 14 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Aisraele afuna kubwerera kunka ku Ejipito

1Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo.

2Eks. 14.11Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!

3Ndipo Yehova atitengeranji kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala chakudya chao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Ejipito?

4Ndipo anati wina ndi mnzake, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Ejipito.

5Num. 16.22Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israele.

6Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zovala zao;

7nanena ndi khamu lonse la ana a Israele, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu.

82Sam. 15.25Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

9Deut. 7.18; 9.7; Mas. 46.11; Yes. 30.2-3Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.

10Eks. 16.10Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'chihema chokomanako kwa ana onse a Israele.

Mose atetezera anthu kwa Mulungu

11 Yoh. 12.37; Aheb. 3.9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?

12Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwachotsera cholowa chao, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu koposa iwowa.

13Ndipo Mose anati kwa Yehova, Pamenepo Aejipito adzamva; popeza munakweza anthu awa ndi mphamvu yanu kuwachotsa pakati pao;

14ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.

15Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti,

16Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa anthu awa m'dziko limene anawalumbirira, chifukwa chake anawapha m'chipululu.

17Ndipo tsopano, ikuletu mphamvu ya Mbuye wanga, monga mudanena, ndi kuti,

18Eks. 20.5; 34.6-7Yehova ndiye wolekereza, ndi wa chifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula wopalamula; wakuwalanga ana chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

19Eks. 32.32Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa chifundo chanu chachikulu, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Ejipito kufikira tsopano.

20Yak. 5.16; 1Yoh. 5.15-16Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako:

21Mas. 72.19koma ndithu, pali Ine, dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova;

22popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;

23Num. 32.11sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;

24koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.

25Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

Odandaulawo saloledwa kulowa dziko la Kanani

26Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati,

27Mat. 17.17Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira.

28Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga;

29mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;

30simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.

31Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala chakudya, amenewo ndidzawalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.

32Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno.

33Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m'chipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m'chipululu.

34Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga chaka chimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.

35Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'chipululu muno, nadzafamo.

36Ndipo amunawo, amene Mose anawatumiza kukazonda dziko, amene anabwera nadandaulitsa khamu lonse pa iye, poipsa mbiri ya dziko,

371Ako. 10.10amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova.

38Num. 26.65Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.

39Ndipo Mose anauza ana a Israele mau onse awa; ndipo anthu anamva chisoni chambiri.

40Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba paphiri, nati, Tili pano, tidzakwera kunka ku malo amene Yehova ananena; popeza tachimwa.

412Mbi. 24.20Ndipo Mose anati, Mutero chifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?

42Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu.

432Mbi. 15.2Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.

44Koma anakwera pamwamba paphiri modzikuza; koma likasa la chipangano la Yehova, ndi Mose, sanachoke kuchigono.

45Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help