1Akadapanda kukhala nafe Yehova,
anene tsono Israele;
2Akadapanda kukhala nafe Yehova,
pakutiukira anthu:
3 Mas. 56.1-2 Akadatimeza amoyo,
potipsera mtima wao.
4Akadatimiza madziwo,
mtsinje ukadapita pa moyo wathu;
5madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu.
6Alemekezedwe Yehova,
amene sanatipereke kumano kwao tikhale chakudya chao.
7 Miy. 6.5 Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi;
msampha unathyoka ndi ife tinaonjoka.
8 Mas. 121.2; 134.3 Thandizo lathu lili m'dzina la Yehova,
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.